1 John 2:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu, zimene mudamva kuyambira pa chiyambi, zikhalebe m'mitima mwanu. Zimene mudamva kuyambira pa chiyambi zikakhalabe m'mitima mwanu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndi mwa Atate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu, cimene munacimva kuyambira paciyambi cikhale mwa Inu, 6 Ngari cikhala mwa inu cimene mudacimva kuyambira paciyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.