1 John 2:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma iye amene akasunga mau ace, mwa iyeyu zedi cikondi ca Mulungu cathedwa. M'menemo tizindikira kuti tiri mwa iye;