1 John 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Zimene lamuloli likunena, zidachitikadi mwa Yesu, ndipo zikuchitikanso mwa inu. Pajatu mdima ulikutha, ndipo kuŵala kwenikweni kwayamba kale kuti ngwee.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndico cimene ciri coona mwa iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala,