1 John 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tisakhale ngati Kaini amene anali wake wa Woipa uja, ndipo adapha mbale wake. Chomuphera chinali chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoipa, koma za mbale wake zinali zolungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
osati monga Kaini anali wocokera mwa woipayo, namupha mbale wace. Ndipo anamupha iye cifukwa ninji? Popeza nchiro zace zinali zoipa, ndi za mbaie wace zolungama.