1 John 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Umo tizindikira cikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wace cifukwa ca ife; ndipo ife tiyener kupereka moyo wathu cifukwa ca abale.