1 John 3:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye amene ali naco coma ca dziko lapansi, naona mbale wace ali wosowa ndi kutsekereza cifundo cace pommana iye, nanga cikondi ca Mulungu cikhala mwa iye bwanji?