1 John 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziŵa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Okondedwa, tsopano riri ana a Mulungu, ndipo sicinaoneke cimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka iye, tidzakhala ofanana ndi iye, Pakuti tidzamuona iye monga ali.