1 John 3:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 6 munthu amene asunga malamulo ace akhala mwa iye, ndi iye mwa munthuyo. Ndipo 7 m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kucokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.