1 John 3:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza kuti umulungu wake wa Mulunguyo uli mwa iye. Sangathe kumachimwirachimwira, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu.