1 John 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati icokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anaturuka kulowa m'dziko lapansi.