1 John 4:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife;