1 John 4:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene chikondi chafikira pake penipeni mwa ife ndi apa pakuti moyo wathu pansi pano uli wonga moyo wa Khristu, kotero kuti tingathe kukhala olimba mtima pa tsiku la chiweruzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.