1 John 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.