1 John 4:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wace, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale ware amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.