1 John 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera;