1 John 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wina akaona mbale wace alikucimwa cimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo iye adzampatsira moyo wa iwo akucita macimo osati a kuimfa. Pali cimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.