1 Kings 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pitani msanga kwa mfumu Davide, mukamfunse kuti, ‘Kodi inu mbuyanga mfumu, suja mudandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu, kuti mwana wanga Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanu nadzakhala pa mpando wanu m'malo mwanu? Nanga chifukwa chiyani Adoniya waloŵa ufumu?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pitani msanga kwa Mfumu Davide ndipo mukanene kuti, ‘Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbire kwa ine mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu mwana wako Solomoni ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwanga, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu?’ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya walowa ufumu?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wadfumu? ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?