1 Kings 1:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene inu muzikalankhula ndi mfumu, inenso ndidzaloŵa pambuyo panu, kuti ndikachitire umboni mau anuwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene inu muzikayankhula ndi mfumu, ine ndidzalowa ndi kuchitira umboni mawu anuwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, uli cilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.