1 Kings 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Bateseba adapita kwa mfumu, nakaloŵa m'chipinda chake. (Apo nkuti mfumuyo itakalamba kotheratu, ndipo Abisagi Msunamu uja ankasamala mfumuyo).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Bateseba analowa kwa mfumu kuchipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Batiseba anapita nakalowa ku chipinda kukaonana ndi mfumu imene inali itakalamba kwambiri, kumene Abisagi wa ku Sunemu uja ankayisamalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Batiseba analowa kwa mfumu kucipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.