1 Kings 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bateseba adati, “Ai nkwabwino. Koma mbuyanga, paja inu mudaandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu m'dzina la Chauta Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanga, nadzakhala pa mpando wanga.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga, inu mwini munalumbira kwa ine mdzakazi wanu mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwa ine, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu.