1 Kings 1:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo wapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndiponso nkhosa zambiri, kuperekera nsembe, ndipo waitana ana anu onse, wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mkulu wankhondo. Solomoni mwana wanu sadamuitaneko ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu kazembe wa nkhondo; koma Solomoni mnyamata wanu sanamuitane.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo wapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndi nkhosa ndi mbuzi ndipo wayitana ana anu onse, wansembe Abiatara ndiponso Yowabu mkulu wa ankhondo, koma sanayitane kapolo wanu Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abyatara wansembe, ndi Yoabu kazembe wa nkhondo; koma Solomo mnyamata wanu sanamuitana.