1 Kings 1:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwakuti tsopano, mbuyanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muŵauze munthu amene adzakhale pa mpando wanu waufumu, m'malo mwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbuye wanga mfumu, maso a Aisraeli onse ali pa inu, kuti adziwe kuchokera kwa inu amene adzakhala pa mpando waufumu wa mbuye wanga mʼmalo mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisrayeli onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye,