1 Kings 1:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adafunsa mfumu kuti, “Mbuyanga mfumu, kodi inu mudalengeza zoti Adoniya ndiye adzakhale mfumu ndi kukhala pampando panu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Natani anafunsa kuti, “Mbuye wanga mfumu, kodi mwalengeza kuti Adoniya adzakhala mfumu mʼmalo mwanu, ndi kuti adzakhala pa mpando wanu waufumu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wacifumu?