1 Kings 1:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti lero lomwe lino wakapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndi nkhosa zambiri, kuperekera nsembe. Ndipo waitana ana anu onse pamodzi ndi Yowabu mkulu wa ankhondo, ndi wansembe Abiyatara. Onsewo akudya ndi kumwa naye Adoniyayo tsopano lino, ndipo akunena kuti, ‘Adzachite kufa ndi ukalamba mfumu Adoniya.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lero lomwe lino wakapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndiponso nkhosa ndi mbuzi. Iye wayitana ana anu onse, atsogoleri a nkhondo, ndiponso wansembe Abiatara. Panopa onsewa akudya ndi kumwa naye ndipo akunena kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Adoniya!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pace, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.