1 Kings 1:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi zimenezi mwalamula ndinu mbuyanga mfumu? Bwanji nanga simudauze anthu anu za mwana amene adzakhale pa mpando wanu waufumu m'malo mwanu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinthu ichi chachitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi zimenezi mbuye wanga mfumu mwazichita ndinu, osawawuza atumiki anu kuti adziwe amene adzakhale pa mpando waufumu mʼmalo mwanu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinthu ici cacitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?