1 Kings 1:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe Chauta wakhalira nanu mbuyanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni, ndipo ufumu wake aukweze ndithu, ngakhale kupambana ufumu wanu, mbuyanga mfumu Davide.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu momwemo akhalenso ndi Solomoni, nakuze mpando wake wachifumu upose mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe Yehova wakhalira ndi inu mbuye wanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni ndi kukhazikitsa ufumu wake kuti ukhale waukulu kuposa ufumu wa mbuye wanga Mfumu Davide!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu, momwemo akhalenso ndi Solomo, nakuze mpando wace wacifumu upose mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.