1 Kings 1:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko wansembe Zadoki adatenga nsupa ya mafuta ya ku hema la Chauta, nadzoza Solomoni. Pomwepo adaliza lipenga, ndipo anthu onsewo adafuula kuti, “Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta yochokera ku malo opatulika ndi kumudzoza Solomoni. Kenaka analiza lipenga ndipo anthu onse anafuwula kuti, “Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Cihema, namdzoza Solomo. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.