1 Kings 1:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Adoniya ndi anthu onse oitanidwa amene anali naye ankamaliza madyerero ao, adalimva phokosolo. Yowabu atamva kulira kwalipenga, adafunsa kuti, “Kodi phokoso limeneli mumzindamo, kwachitikanji?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yowabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi chiyani kuti m'mudzi muli chibumo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adoniya pamodzi ndi anthu onse oyitanidwa amene anali naye anamva zimenezi pamene ankamaliza madyerero awo. Atamva kulira kwa malipenga, Yowabu anafunsa kuti, “Kodi phokoso lonselo mu mzindamo likutanthauza chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yoabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi ciani kuti m'mudzi muli cibumo?