1 Kings 1:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo anthu onse amene Adoniya adaaŵaitana aja adayamba kunjenjemera, ndipo adamwazikana aliyense kumapita kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anachita mantha, nanyamuka, napita yense njira yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse amene Adoniya anawayitana ananjenjemera ndi mantha, ndipo anayimirira, kenaka anamwazikana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anacita mantha, nanyamuka, napita yense njira yace.