1 Kings 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, adayamba kudzikuza namanena kuti, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Motero adadzipezera magaleta ndi anthu okwera pa akavalo, ndiponso anthu operekeza makumi asanu oti azithamanga patsogolo pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi Adoniya, mwana wa Hagiti, anayamba kudzitukumula ndipo anati, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Choncho anadzikonzera galeta ndi akavalo, pamodzi ndi anthu 50 woti azithamanga patsogolo pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agareta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.