1 Kings 1:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ena adauza Solomoni kuti, “Adoniya akukuwopani, inu mfumu Solomoni, ndipo wakagwira nsonga za guwa lansembe, ndipo akunena kuti poyamba afuna kuti inu mfumu Solomoni mulumbire kuti simudzamupha mtumiki wanuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anakauza Solomoni, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomoni, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomoni alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wake ndi lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Solomoni anawuzidwa kuti, “Adoniya akukuopani inu Mfumu Solomoni ndipo wagwira msonga za guwa lansembe. Iye akuti, ‘Mfumu Solomoni alumbire kuti sadzapha kapolo wake ndi lupanga.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anakauza Solomo, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomo, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomo alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wace ndi lupanga.