1 Kings 1:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adati, “Iyeyo akakhala womvera, sitimchita choipa chilichonse, koma akakhala woipa mtima, adzafa basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anayankha kuti, “Ngati iyeyo aonetse kuti ndi munthu wakhalidwe labwino, ngakhale tsitsi la mʼmutu mwake silidzathothoka ndi kugwera pansi, koma akapezeka kuti ali ndi khalidwe loyipa, adzafa ndithu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anati, iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lace limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye coipa, adzafadi.