1 Kings 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso mneneri Natani, Simei, Rei, pamodzi ndi anthu amphamvu aja a Davide, sadamtsate Adoniyayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Zadoki wansembe, Benaya mwana wa Yehoyada, mneneri Natani, Simei ndi Rei ndiponso asilikali amphamvu a Davide sanamutsate Adoniya uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wace wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simeyi, ndi Reyi, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.