1 Kings 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Adoniya adapereka nsembe za nkhosa, ng'ombe ndiponso anaang'ombe onenepa ku Mwala wa Njoka umene uli pafupi ndi Enirogele. Adaitana abale ake onse, ana a mfumu, ndi akazembe onse a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Adoniya anapereka nsembe za nkhosa ndi ngʼombe ndiponso ana angʼombe onenepa ku Mwala wa Zohereti kufupi ndi Eni Rogeli. Iye anayitana abale ake onse, ana aamuna a mfumu ndiponso akuluakulu onse a ku Yuda,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi citsime ca Rogeli, naitana abale ace onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anayamata a mfumu;