1 Kings 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni yobukitsa dzina la Chauta, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.