1 Kings 10:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitengo imeneyo mfumuyo idasemera mizati yochirikizira Nyumba ya Chauta ndi ina yochirikizira nyumba yachifumu. Adasemanso azeze ndi apangwe a anthu oimba. Panalibe mitengo yotere imene idabweranso kapena kuwonekanso mu Israele mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oyimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa.