1 Kings 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
osaŵerengera amene ankabwera ndi alendo ndi anthu amalonda, ndiponso wina wochokera kwa mafumu onse a ku Arabiya, ndi kwa nduna zam'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabu, ndi wa akazembe onse a madera.