1 Kings 10:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu asanu ndi awiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri zagolide wonsansantha, chikopa chimodzi chinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Solomo anapanga zikopa mazana awiri zagolidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi.