1 Kings 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira kilogramu limodzi ndi theka. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, lihawo limodzi linapangidwa ndi miyeso ya mina itatu ya golide; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, libawo limodzi linapangidwa ndi miyeso itatu ya golidi; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.