1 Kings 10:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndipo chosamira chake unali woulungika pamwamba. Mpandowo unali ndi chosanjikapo manja uku ndi uku, ndipo zifanizo ziŵiri za mikango itaima pambali pa zosanjikapo manjazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mpandowo wachifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wachifumu panali pozunguniza kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mpandowo wacifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wacifumu panali pozungulira kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.