1 Kings 10:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wace waukulu, ndi ngamila zakunyamula zonunkhira, ndi golidi wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.