1 Kings 10:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide. Ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Panalibe zasiliva popeza kuti silivayo sanali kanthu pa nthaŵi ya Solomoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomo zinali zagolidi, ndi zotengera zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali zagolidi yekha yekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva ana ngoyesedwa opanda pace masiku onse a Solomo.