1 Kings 10:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu inali ndi zombo zochokera ku Tarisisi zimene zinkayenda pa nyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu; ndipo chaka chachitatu chilichonse zinkabwera zitanyamula golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisisi zinafika kamodzi zitapita zaka zitatu, zili nazo golide, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisi zinafika, kamodzi zitapita zaka zitatu, ziri nazo golidi, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za maanga maanga.