1 Kings 10:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inachulukitsa siliva ngati miyala m'Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inacurukitsa siliva ngati miyala m'Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo.