1 Kings 10:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo kavalo pa mtengo wa masekeli asiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya, nawonso ankhagula zinthuzo kudzera mwa anthu amalonda omwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo galeta limodzi linachokera kutuluka m'Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo gareta limodzi linacokera kuturuka m'Aigupto mtengo wace masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wace masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.