1 Kings 10:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndi kuziwona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiwuze zonse, ngakhale ndi theka lomwe. Nzeru zanu ndiponso zabwino zimene muli nazo zikuposa zimene ndinkazimva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sindinakhulupirira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sindinakhulupira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.