1 Kings 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando waufumu wa dziko la Israele. Chifukwa choti Chauta adakonda Israele mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wacifumu wa Israyeli; popeza Yehova anakonda Israyeli nthawi yosatha, cifukwa cace anakulongani inu ufumu, kuti mucite ciweruzo ndi cilungamo.