1 Kings 11:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Solomoni ankakonda akazi ambiri achilendo. Kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, adakwatiranso akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni ndi Ahiti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Solomo anakonda akazi ambiri acilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Moabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Zidoni, ndi Ahiti;