1 Kings 11:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe sindidzalanda ufumu wonse. Mwana wako ndidzamsiyirako fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndidausankha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe sindidzamulanda ufumu wonse, koma ndidzamusiyira fuko limodzi chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
komatu sindidzacotsa ufumu wonsewo; pfuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi cifukwa ca Yerusalemu amene ndinamsankha.