1 Kings 11:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Hadadi adaathaŵira ku Ejipito pamodzi ndi Aedomu ena, atumiki a bambo wake. Pamenepo nkuti Hadadiyo ali mwana wamng'ono.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wake pamodzi naye, kunka ku Ejipito, Hadadiyo akali mwana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wace pamodzi naye, kumka ku Aigupto, Hadadiyo akali mwana.